Cibvumbulutso 14 BL92

Mwanawankhosa ndi oomboledwa ace pa phiri la Ziyoni

1 Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lace ndi dzina la Atate wace lolembedwa pamphumi pao.

2 Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ngati mkokomo wamadzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikuru; ndipo mauamene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuyimba azeze ao j

3 ndipo ayimba ngati nyimbo yatsopane ku mpando wacifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, kama zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kucokera kudziko.

4 Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukulakwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

5 Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwa bodza; ali opanda cirema.

Angelo atatu akulalikiratu ziweruziro za Mulungu

6 Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uti wonse ndi pfuko ndi manenedwe ndi anthu j

7 ndi kunena ndi mau akuru, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya ciweruziro cace; ndipo mlambireni iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi,

8 Ndipo anatsata mngelo wina mnzace ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace.

9 Ndipo anawatsata mngelo wina, wacitatu, nanena ndi mau akuru, Ngati wina alambira ciromboco, ndi fane lace, nalandira lembapamphumi pace, kapena pa dzanja lace,

10 iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'cikho ca mkwiyo wace; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa j

11 ndipo utsi wa kuzunza kwao tukwera ku nthawiza nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku: iwo akulambira ciromboco ndi fano lace, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lace.

12 Pano pali cipiriro ca oyera mtima, ca iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi cikhulupiriro ca Yesu.

13 Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.

Masika a dzinthu ndi a mphesa

14 Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa munthu, wakukhala naye korona wagolidi pamutu pace, ndi m'dzanja lace zenga lakuthwa.

15 Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi, wopfuulandi mau akuru kwa iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zacetsa.

16 Ndipo iye wokhala pamtambo anaponya zenga lace padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.

17 Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi ali m'Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso.

18 Ndipo mngelo wina anaturuka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; napfuula ndi mau akuru kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, 1 Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zace zapsa ndithu.

19 Ndipo mngelo anaponya zenga lace ku dziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, 2 naziponya moponderamo mphesa mwamukuru mwa mkwiyo wa Mulungu.

20 Ndipo 3 moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mudzi, ndipo mudaturuka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya cikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22