Cibvumbulutso 3 BL92

Kalata wacisanu, wa kwa Mpingo wa ku Sarde

1 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sarde lemba:Izi anena iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi riwiri: Ndidziwa nchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.

2 Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira, zimene zinafuna kufa; pakutisindinapeza nchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.

3 Cifukwa cace kumbukila umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yace ndidzadza pa iwe.

4 Komatu uli nao maina owerengeka m'Sarde, amene sanadetsa zobvala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; cifukwa ali oyenera.

5 Iye amene alakika adzambveka motero zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lace m'buku la moyo, ndipo ndidzambvomereza dzina lace pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ace.

6 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata wacisanu ndi cimodzi, wa kwa Mpingo wa ku Filadelfeya

7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfeya lemba;Izi anena iye amene ali Woyera, iye amene ali Woona, iye wakukhala naco cifungulo ca Davide, iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:

8 Ndidziwa nchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.

9 Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

10 Popeza unasunga mau a cipiriro canga, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

11 Ndidza msanga; gwira cimene uli naco, kuti wina angalande korona wako.

12 Iye wakulakika, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kacisi wa Mulungu wanga, ndipo kuturuka sadzaturukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kucokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.

13 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Kalata wacisanu ndi ciwiri, wa kwa Mpingo wa ku Laodikaya

14 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikaya lemba:Izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa cilengo ca Mulungu:

15 Ndidziwa nchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

16 Kotero, popeza uti wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m'kamwa mwanga.

17 Cifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo cuma ndiri naco, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wocititsa cifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

18 ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m'moto, kuti ukakhale wacuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadzibveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

19 Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.

20 Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

21 Iye wakulakika, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wacifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wacifumu wace.

22 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22