Cibvumbulutso 17 BL92

Kupasuka kwa Babulo. Cirombo cisokeretsa mkazi wacigololo

1 Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa citsutso ca mkazi wacigololo wamkuru, wakukhala pa madzi ambiri,

2 amene mafumu a dziko anacita cigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa cigololo cace.

3 Ndipo ananditenga kumka nane kucipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pacirombo cofiiritsa, codzala ndi maina a mwano, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

4 Ndipo mkazi anabvala cibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wace, ndi ngale; nakhala naco m'dzanja lace cikho cagolidi codzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za cigololo cace,

5 ndipo pamphumi pace padalembedwa dzina, CINSINSI, BABULO WAUKURU AMAI WA ACIGOLOLO NDI WA ZONY ANSITSA ZA DZIKO.

6 Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukuru.

7 Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa cifukwa ninji? ine ndidzakuuza iwe cinsinsi ca mkazi, ndi ca cirombo cakumbereka iye, cokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

8 Cirombo cimene unaciona cinaliko, koma kulibe; ndipo cidzaturuka m'phompho, ndi kunka kucitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo ciyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona cirombo, kuti cinaliko, ndipo kulibe, ndipo cidzakhalako.

9 Pano pali mtima wakukhaia nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;

10 ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iriko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi.

11 Ndipo cirombo cinalico, ndi kulibe, ico comwe nelieo cacisanu ndi citatu, ndipo ciri mwa zisanu ndi ziwirizo, nicimuka kucitayiko.

12 Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi cirombo.

13 Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa cirombo.

14 Iwo adzacita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, cifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.

15 Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wacigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.

16 Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi cirombo, izi zidzadana ndi mkazi wacigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yace, nizidzampsereza ndi moto.

17 Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kucita za m'mtima mwace, ndi kucita ca mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa cirombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.

18 Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukuru, wakucita ufumu pa mafumu a dziko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22