Cibvumbulutso 22 BL92

1 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, oturuka ku mpando wacifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawarikhosa.

2 Pakati pa khwalala lace, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lace lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zace mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuciritsa nao amitundu.

3 Ndipo sipadzakhalanso temberero liri lonse; ndipo mpando wacifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ace adzamtumikira iye,

4 nadzaona nkhope yace; ndipo dzina lace lidzakhala pamphumipao.

5 Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; cifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzacita ufumu ku nthawi za nthawi.

Macenjezo ndi malonjezano

6 Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wace kukaonetsera akapolo ace zimene ziyenera kucitika msanga.

7 Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a cinenero ca buku ili.

8 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.

9 Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usacite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.

10 Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza cizindikilo mau a cinenero ca buku ili; pakuti nthawi yayandikira.

11 Iye wakukhala wosalungama acitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama acitebe colungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.

12 Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa nchito yace.

13 Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, ciyambi ndi citsiriziro.

14 Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.

15 Kunja kuli agaru ndi anyanga, ndi acigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulicita.

16 Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukucitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzo ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.

17 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani, Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.

18 Ndicita umboni kwa munthu ali yense wakumva mau a cinenero ca buku ili, 1 Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu:

19 ndipo 2 ali yense akacotsako pa mau a buku la cinenero ici, Mulungu adzamcotsera gawo lace pa mtengo wa moyo, ndi 3 m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.

20 Iye wakucitira umboni izi, anena, 4 Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.

21 5 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi oyera mtima onse, Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22