Cibvumbulutso 21 BL92

Miyamba yatsopano ndi dziko latsopano

1 Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidaeoka, ndipo kulibenso nyanja.

2 Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wace.

3 Ndipo ndinamva mau akuru ocokera ku mpando wacifumu, ndi kunena Taonani, cihema ca Mulungu ciri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ace, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;

4 ndipo adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.

5 Ndipo Iye wakukhala pa mpando wacifumu anati, Taonani, ndicita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.

6 Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe ku kasupe wa madzi a moyo kwaulere.

7 Iye wakulakika adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wace, ndi iye adzakhala mwana wanga.

8 Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.

Yerusalemu watsopano

9 Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu Ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.

10 Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka ku phiri lalikuru ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika m'Mwamba kucokera kwa Mulungu,

11 ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwace kunafanana ndi mwala wa mtengo wace woposa, Dgati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;

12 nukhala nalo linga lalikuru ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi mama olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israyeli;

13 kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwela zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.

14 Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

15 Ndipo iye wakulankhula ridi ine anali nao muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zace, ndi linga lace.

16 Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.

17 Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.

18 Ndipo mirimo ya linga lace ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.

19 Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu; mazikooyamba, ndi yaspi; aciwiri, ndi safiro; acitatu, ndi kalikedo; acinai, ndi smaragido;

20 acisanu, ndi sardoau; acisanu ndi cimodzi, ndi sardiyo; acisanu ndi ciwiri, ndi krusolito; acisanu ndi citatu, ndi berulo; acisanu ndi cinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndt cimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi ciwiri, ndi ametusto.

21 Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; citseko ciri conse pa cokha ca ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda ma golidi woyengeka, ngati mandala openyekera.

22 Ndipo siridinaona Kacisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kacisi wace.

23 Ndipo 1 pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yace ndiye Mwanawankhosa.

24 Ndipo 2 amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwace; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.

25 Ndipo 3 pa zipata zace sipatsekedwa konse usana, 4 (pakuti sikudzakhala usiku komweko);

26 ndipo 5 adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo;

27 ndipo 6 simudzalowa konse momwemo kanthu kali konse kosapatulidwa kapena iye wakucita conyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa 7 m'buku la moyo la Mwanawankhosa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22