Cibvumbulutso 11 BL92

Mboni ziwirt

1 Ndipoanandipatsa ine bango ngati ndodo, ndikuti, Tanyamuka, nuyese Kacisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.

2 Ndipo bwalo la kunja kwa Kacisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.

3 Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zobvala ciguduli.

4 Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

5 Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto uturuka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ace ayenera kutero.

6 Izo ziti nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a cinenero cao; ndipo ulamuliro ziti nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi iri yonse zikafuna.

7 Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao cirombo eokwera kuturuka m'phompho cidzacita nazo nkhondo, nicidzazilaka, nicidzazipha izo.

8 Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala la mudzi waukuru, umene uchedwa, ponena zacizimu, Sodoma ndi Aigupto, pameneponso Ambuye wao anapacikidwa.

9 Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lace, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.

10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.

11 Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lace mzimu wamoyo wocokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala ciriri; ndipomantha akuru anawagwera iwo akuwapenya.

12 Ndipo anamva mau akuru akucokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.

13 Ndipo panthawipo panali cibvomezi cacikuru, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi Iidagwa; ndipo anaphedwa m'cibvomezico anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.

14 Tsoka laciwiri lacoka; taonani, tsoka lacitatu lidza msanga.

Lipenga lotsiriza

15 Ndipo mngelo wacisanu ndi ciwiri anaomba, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wace: ndipo adzacita ufumu kufikira nthawi za nthawi.

16 Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yacifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,

17 nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru, ndipo mwacita ufumu.

18 Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akuru; ndi kuononga iwo akuononga dziko.

19 Ndipo anatsegulidwa Kacisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la cipangano cace, m'Kacisi mwace, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi cibvomezi, ndi matalala akuru.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22