Cibvumbulutso 12 BL92

Za mkazi ndi cinjoka

1 Ndipo cizindikilo cacikuru cinaoneka m'mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa, ndi mwezi ku mapazi ace, ndi pamutu pace korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;

2 ndipo anali ndi pakati; ndipo apfuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.

3 Ndipo cinaoneka cizindikilo cina m'mwamba, taonani, cinjoka cofiira, cacikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zacifumu zisanu ndi ziwiri.

4 Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.

5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wacifumu wace.

6 Ndipo mkazi anathawira kucipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

7 Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi cinjoka; cinjokanso ndi angelo ace cinacita nkhondo;

8 ndipo sicinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba.

9 Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.

10 Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.

11 Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.

12 Cifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.

13 Ndipo pamene cinjoka cinaonakuticinaponyedwa pansikudziko, cinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.

14 Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a ciombankhanga cacikuru, kuti akaulukire kucipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.

15 Ndipo inalabvulira m'kamwa mwace, potsata mkazi, madzi ngati mtsinje, kuti akakokoleredwe mkazi nao.

16 Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwace, nilinameza madzi a mtsinje amene cinjoka cinalabvula m'kamwamwace.

17 Ndipo cinjoka cinakwiya ndi mkazi, nicinacoka kunka kucita nkhondondi otsala ambeu yace, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22