1 Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi ciwiri, munali cete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.
2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.
3 Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.
4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi mota wopara pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi cibvomezi.
6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.
7 Ndipo woyamba anaomba, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.
8 Ndipo mngelo waciwiri anaomba, ndipo monga ngati phiri lalikuru lakupserera ndi mota Iinaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;
9 ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa ziri m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.
10 Ndipo anaomba mngelo wacitatu, ndipo idagwa kucokera kumwamba nyenyezi yaikuru, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;
11 ndipo dzina lace la nyenyeziyo alicha Cowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka cowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti anasanduka owawa.
12 Ndipo mngelo wacinai anaomba, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ace atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.
13 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva ciombankhanga cirikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akuru, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padz'ko, cifukwa ca mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.