3 Mulungu anafuma ku Temani,Ndi Woyerayo ku phiri la Parana.Ulemerero wace unaphimba miyamba,Ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
4 Ndi kunyezimira kwace kunanga kuunika;Anali nayo mitsitsi ya dzuwa yoturuka m'dzanja lace.Ndi komweko kunabisika mphamvu yace.
5 Patsogolo pace panapita mliri,Ndi makara amoto anaturuka pa mapaziace.
6 Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;Anapenya, nanjenjemeretsa amitundu;Ndi mapiri acikhalire anamwazika,Zitunda za kale lomwe zinawerama;Mayendedwe ace ndiwo a kale lomwe.
7 Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;Nsaru zocinga za dziko la Midyani zinanjenjemera.
8 Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,Kapena ukali wanu panyanja,Kuti munayenda pa akavalo anu,Pa magareta anu a cipulumutso?
9 Munapombosola uta wanu;Malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.