1 Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!Wagwetsa pansi kucokera kumwamba kukoma kwace kwa Israyeli;Osakumbukira poponda mapazi ace tsiku la mkwiyo wace.
2 Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.
3 Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli;Wabweza m'mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo,Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.
4 Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;Wapha onse okondweretsa maso;Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.