Maliro 3 BL92

Yeremiya acita nkhawa, adziponya kwa Yehova

1 Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wace.

2 Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m'kuunika ai.

3 Zoonadi amandibwezera-bwezera dzanja lace monditsutsa tsiku lonse.

4 Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa, natyola mafupa anga.

5 Wandimangira zitando za nkhondo, wandizinga ndi ulembe ndi mabvuto.

6 Wandikhalitsa mumdima ngati akufakale.

7 Wanditsekereza ndi guta, sindingaturuke; walemeretsa unyolo wanga.

8 Inde, popfuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa.

9 Watsekereza njira zanga ndi miya la yosema, nakhotetsa mayendedwe anga.

10 Andikhalira cirombo colalira kapena mkango mobisalira.

11 Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.

12 Wathifula uta wace, nandiyesa polozetsa mubvi.

13 Walowetsa m'imso mwanga mibvi ya m'phodo mwace.

14 Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse, ndi nyimbo yao tsiku lonse.

15 Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa civumulo.

16 Watyolanso mano anga ndi tinsangalabwi, wandikuta ndi phulusa.

17 Watarikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.

18 Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova.

19 Kumbukirani msauko Wanga ndi kusocera kwanga, ndizo civumulo ndi ndulu.

20 Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine,

21 Ndiri naco ciyembekezo popeza ndilingalira ici ndiyembekeza kanthu.

22 Cifukwa cakusathedwa ife ndico cifundo ca Yehova, pakuti cisoni cace sicileka;

23 Cioneka catsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

24 Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; cifukwa cace ndidzakhulupirira.

25 Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.

26 Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

27 Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng'ono.

28 Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.

29 Aike kamwa lace m'pfumbi; kapena ciripo ciyembekezo.

30 Atembenuzire wompanda tsaya lace, adzazidwe ndi citonzo.

31 Pakuti Yehova sadzataya kufikira nthawi zonse,

32 Angakhale aliritsa, koma adzacitira cisoni monga mwa kucuruka kwa zifundo zace.

33 Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu cisoni.

34 Kupondereza andende onse a m'dziko,

35 Kupambutsa ciweruzo ca munthu pamaso pa Wam'mwambamwamba,

36 Kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda.

37 Ndani anganene, conena cace ndi kucitikadi, ngati Ambuye salamulira?

38 Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba simuturuka zobvuta ndi zabwino?

39 Kodi munthu wamoyo adandauliranji pokhala m'zocimwa zace?

40 Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova.

41 Titukulire mitima yathu ndi, manja athu omwe kwa Mulungu ali kumwamba.

42 Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukira.

43 Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola, mwatipha osacitira cisoni.

44 Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.

45 Mwatiika pakati pa amitundu ngati zinyalala ndi za kudzala.

46 Adani athu onse anatiyasamira,

47 Mantha ndi dzenje zitifikira, ndiphokose ndi cionongeko.

48 M'diso mwanga mutsikamitsinje ya madzi cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga woonongedwa,

49 Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula,

50 Kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona;

51 Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa cifukwa ca ana akazi onse a m'mudzi mwanga.

52 Ondida opanda cifukwa anandiinga ngati mbalame;

53 Anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwambapaine;

54 Madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, dalikhidwa.

55 Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndiri m'dzenje lapansi;

56 Munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi popfuulaine.

57 Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.

58 Ambuye munanenera moyo wanga mirandu yace; munaombola moyo wanga.

59 Yehova, mwaona coipa anandicitiraco, mundiweruzire;

60 Mwaona kubwezera kwao konse ndi zopangira zao zonse za pa ine.

61 Mwamva citonzo cao, Yehova, ndi zopangira zao zonse za pa ine,

62 Milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.

63 Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.

64 Mudzawabwezera cilango, Yehova, monga mwa macitidwe a manja ao;

65 Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;

66 Mudzawalondola mokwiya ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5