Maliro 4 BL92

Tsoka a anthu Avuda

1 Ha! golidi wagugadi; golidi woona woposa wasandulika;Miyala ya malo opatulika yakhutulidwa pa malekezero a makwalalaonse.

2 Ana a Ziyoni a mtengo wapatari, olingana ndi golidi woyengetsa,Angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

3 Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;Koma mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'cipululu.

4 Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwace ndi ludzu;Ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

5 Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;Omwe analeredwa nabvekedwa mlangali afungatira madzala.

6 Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga, ikula koposa cimo la Sodomu,Umene unapasuka m'kamphindi, anthu osaucitira kanthu.

7 Omveka ace anakonzeka koposa cipale cofewa, nayera koposa mkaka,Matupi ao anafiira koposa timiyala toti pyu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatari.

8 Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala;Khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.

9 Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala;Pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.

10 Manja a akazi acisoni anaphika anaanao;Anali cakudya cao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

11 Yehova wakwaniritsa kuzaza kwace, watsanulira ukali wace;Anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ace,

12 Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirira, ngakhale onse okhala kunja kuno,Kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.

13 Ndico cifukwa ca macimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembeace,Amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pace.

14 Asocera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi;Anthu sangakhudze zobvala zao.

15 Amapfuula kwa iwo, Cokani, osakonzeka inu, cokani, cokani, musakhudze kanthu.Pothawa iwo ndi kusocera, anthu anati mwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.

16 Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;Iwo sanalemekeza ansembe, sanakomera mtima akulu.

17 Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo cabe;Kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.

18 Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;Citsiriziro cathu cayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti citsiriziro cathu cafikadi.

19 Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwilo lao,Anatithamangitsa pamapiri natilalira m'cipululu.

20 Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; Amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwace pakati pa amitundu,

21 Kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dzikola Uzi;Cikho cidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kubvulazako.

22 Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende;Koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzabvumbulutsa zocimwa zako.

Mitu

1 2 3 4 5