Maliro 2 BL92

Yerusalemu amangidwa misasa, njala isautsa, mudzi upasuka

1 Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!Wagwetsa pansi kucokera kumwamba kukoma kwace kwa Israyeli;Osakumbukira poponda mapazi ace tsiku la mkwiyo wace.

2 Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazicitira cisoni;Wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wace;Wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ace.

3 Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli;Wabweza m'mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo,Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.

4 Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo;Wapha onse okondweretsa maso;Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.

5 Yehova wasanduka mdani, wameza Israyeli;Wameza zinyumba zace zonse, wapasula malinga ace;Nacurukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi cibumo.

6 Wacotsa mwamphamvu dindiro lace ngati la m'munda;Waononga mosonkhanira mwace;Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi sabata m'Ziyoni;Wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.

7 Ambuye wataya guwa lace la nsembe, malo ace opatulika amnyansira;Wapereka m'manja a adani ace makoma a zinyumba zace;Iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.

8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni;Watambalika cingwe, osabweza dzanja lace kuti lisaonongepo;Waliritsa chemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

9 Zipata zace zalowa pansi; waononga ndi kutyola mipiringidzo yace;Mfumu yace ndi akalonga ace ali pakati pa amitundu akusowa cilamulo;Inde, aneneri ace samalandira masomphenya kwa Yehova.

10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.

11 Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga;Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.

12 Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.

13 Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?

14 Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa;Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.

15 Onse opita panjira akuombera manja:Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?

16 Adani ako onse ayasamira pa iwe, Atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;Ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.

17 Yehova wacita comwe analingalira;Watsiriza mau ace, amene analamulira nthawi yakale;Wagwetsa osacitira cisoni;Wakondweretsa adani pa iwe,Wakweza nyanga ya amaliwongo ako.

18 Mtima wao unapfuula kwa Ambuye,Linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;Usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

19 Tauka, tapfuula usiku, poyamba kulonda;Tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;Takwezera maso ako kwa Iye, cifukwa ca moyo wa tiana tako,Timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.

20 Onani Yehova, nimupenye, mwacitira ayani ici?Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawaseweza?Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?

21 Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala;Anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;Munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osacitira cisoni.

22 Mwaitana zondiopsya mozungulira ngati tsiku la msonkhano;Panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;Omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.

Mitu

1 2 3 4 5