15 Cimwemwe ca mtima wathu calekeka,Masewera athu asanduka maliro.
16 Korona wagwa pamutu pathu;Kalanga ife! pakuti tinacimwa.
17 Cifukwa ca ici mtima wathu ufoka,Cifukwa ca izi maso athu acita cimbuuzi;
18 Pa phiri la Ziyoni lopasukaloAnkhandwe ayendapo.
19 Inu, Yehova, mukhala cikhalire,Ndi mpando wanu wacifumu ku mibadwo mibadwo.
20 Bwanji mutiiwala ciiwalire,Ndi kutisiya masiku ambirimbiri;
21 Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi,Mukonzenso masiku athu ngati kale lija.