2 Colowa cathu casanduka ca alendo,Ndi nyumba zathu za acilendo.
3 Ndife amasiye opanda atate,Amai athu akunga akazi amasiye.
4 Tinamwa madzi athu ndi ndalama,Tiona nkhuni zathu pozigula.
5 Otilondola atigwira pakhosi pathu,Tatopa osaona popumira.
6 Tinagwira mwendo AiguptoNdi Asuri kuti tikhute zakudya.
7 Atate athu anacimwa, kulibe iwo;Ndipo tanyamula mphulupulu zao.
8 Akapolo atilamulira;Palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.