9 Timalowa m'zoopsya potenga zakudya zathu,Cifukwa ca lupanga la m'cipululu,
10 Khungu lathu lapserera ngati pamotoCifukwa ca kuwawa kwa njala.
11 Anaipitsa akazi m'Ziyoni,Ndi anamwali m'midzi ya Yuda.
12 Anawapacika akalonga manja ao;Sanalemekeza nkhope za akulu.
13 Anyamata ananyamula mphero,Ana nakhumudwa posenza nkhuni.
14 Akulu adatha kuzipata,Anyamata naleka nyimbo zao.
15 Cimwemwe ca mtima wathu calekeka,Masewera athu asanduka maliro.