13 Manga gareta ku kavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kucimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israyeli zinapezedwa mwa iwe.
14 Cifukwa cace pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti Gati; nyumba za Akizibi zidzakhala cinthu cabodza kwa mafumu a Israyeli.
15 Ndidzakutengeranso wokhala m'Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale colowa cace; ulemerero wa Israyeli udzafikira ku Adulamu.
16 Udziyeseze wadazi, udzimete wekha cifukwa ca ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakucokera, nalowa ndende.