5 Anthu anga, kumbukilanitu cofunsira Balaki mfumu ya Moabu, ndi comuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.
6 Ndidzafika kwa Yehova ndi ciani, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi ana a ng'ombe a caka cimodzi?
7 Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba cifukwa ca kulakwa kwanga, cipatso ca thupi langa cifukwa ca kucimwa kwa moyo wanga?
8 Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?
9 Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.
10 Kodi m'nyumba ya woipa mukali cuma cosalungama, ndi muyeso wocepa umene ayenera kuipidwa nao?
11 Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?