5 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.
6 Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amace, mpongozi aukira mpongozi wace; adani ace a munthu ndiwo a m'nyumba yace.
7 Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa cipulumutso canga; Mulungu wanga adzandimvera.
8 Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.
9 Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, cifukwa ndamcimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditurutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya cilungamo cace.
10 Pamenepo mdani wanga adzaciona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.
11 Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzacotsedwa kunka kutali.