1 Ndipo Naomi anali nave mbale wa mwamuna wace, ndiye munthu mwini cuma cambiri wa banja la Elimeleki; dzina lace ndiye Boazi.
2 Nati Rute Mmoabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha is ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomeramtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.
3 Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ocekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Boazi, ndiye wa banja la Elimeleki.
4 Ndipo taona, Boazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa oceka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.