1 Pamenepo Naomi mpongozi wace ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?
2 Nanga Boazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ace? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.
3 Usambe tsono, nudzole, nubvale zobvala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.
4 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nubvundukule ku mapazi ace, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kucita iwe.