1 NDIPO mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti,
2 Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti coipa cao candikwerera pamaso panga.
3 Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako combo comuka ku Tarisi, napereka ndalama zace, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova.
4 Koma Yehova anautsa cimphepo cacikuru panyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi combo cikadasweka.
5 Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato.
6 Ndipo mwini combo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukila tingatayike.
7 Ndipo anati yense kwa mnzace, Tiyeni ticite maere, kuti tidziwe coipa ici catigwera cifukwa ca yani. M'mwemo anacita maere, ndipo maere anagwera Yona.