13 Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao.
14 Pamenepo anapfuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike cifukwa ca moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosacimwa; pakuti, Inu Yehova, mwacita monga mudakomera Inu.
15 Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwace.
16 Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi manthaakuru, namphera Yehova nsembe, nawinda.
17 Koma Yehova anaikiratu cinsomba cacikuru cimeze Yona; ndipo Yona anali m'miroba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.