19 Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ace, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale citonzo mwa amitundu;
20 koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.
21 Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wacita zazikuru.
22 Musamaopa, nyama za kuthengo inu; pakuti m'cipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.
23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa cilungamo cace; nakubvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba.
24 Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.
25 Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi cirimamine, ndi anoni, ndi cimbalanga, gulu langa lalikuru la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.