7 Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda liri lonse njira yace, osasokonezeka m'mabande ao.
8 Sakankhana, ayenda liri lonse m'mopita mwace; akagwa m'zida, siityoka nkhondo yao.
9 Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati mkhungu.
10 Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zi'bweza kuwala kwao;
11 ndipo Yehova amveketsa mau ace pamaso pa khamu lace la nkhondo; pakuti a m'cigono mwace ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakucita mau ace ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikuru ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?
12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kucita maliro;
13 ndipo ng'ambani mitima yanu, si zobvala zanu ai; ndi kurembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wacisomo, ndi wodzala cifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wocuruka kukoma mtima, ndi woleka coipaco.