1 Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu,
2 ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao ku cigwa ca Yosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi colowa canga Israyeli, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa,
3 Ndipo anacitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.
4 Ndiponso ndiri ndi ciani ndi inu, Turo ndi Zidoni, ndi malire onse a Afilisti? mudzandibwezera cilango kodi? Mukandibwezera cilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera cilango canu pamutu panu,
5 Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golidi wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akacisi anu;
6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwacotsa kutali kwa malire ao;