5 Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golidi wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akacisi anu;
6 munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwacotsa kutali kwa malire ao;
7 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera cilango canu pamutu panu;
8 ndipo ndidzagulitsa ana ako amuna ndi akazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutari; pakuti Yehova wanena.
9 Mulalikire ici mwa amitundu mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
10 Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo; wofoka anene, Ndine wamphamvu.
11 Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.