10 Kucokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera naco copereka canga.
11 Tsiku ilo sudzacita manyazi ndi zocita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzacotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzacita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.
12 Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.
13 Otsala a Israyeli sadzacita cosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
14 Yimba, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.
15 Yehova wacotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso coipa.
16 Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.