1 PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu: Cisomo kwa inu ndi mtendere.
2 Tiyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu nonse, ndi kukumbukila inu m'mapemphero athu;
3 ndi kukumbukila kosalekeza nchito yanu ya cikhulupiriro, ndi cikondi cocitacita, ndi cipiriro ca ciyembekezo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;
4 podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, cisankhidwe canu,
5 kuti Vthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kucuruka kwakukuru; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu cifukwa ca inu.
6 Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'cisautso cambiri, ndi cimwemwe ca Mzimu Woyera;