4 komatu monga Mulungu anatibvomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.
5 Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iri yonse, monga mudziwa, kapena kupsiniira msiriro, mboni ndi Mulungu;
6 kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsanl monga atumwi a Kristu.
7 Komatu tinakhala ofat sa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ace a iye yekha;
8 kotero ife poliralira inu, tinabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.
9 Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.
10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;