6 kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsanl monga atumwi a Kristu.
7 Komatu tinakhala ofat sa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ace a iye yekha;
8 kotero ife poliralira inu, tinabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.
9 Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.
10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;
11 monga mudziwa kuti tinacitira yense wa inu pa yekha, monga atate acitira ana ace a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kucita umboni,
12 kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wace wa iye yekha, ndi ulemerero.