1 Cotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, eurukani koposa momwemo.
2 Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.
3 Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;
4 yense wa inu adziwe kukhala naco cotengera cace m'ciyeretso ndi ulemu,