1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani,
2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku,
3 Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
4 Kama inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;