1 PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,
2 monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.
3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa cifundo cace cacikuru, anatibalanso ku ciyembekezo ca moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu;
4 kuti tilandire colowa cosabvunda ndi cosadetsa ndi cosafota, cosungikira m'Mwamba inu,
5 amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa cikhulupiriro, kufikira cipulumutso cokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
6 M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,
7 kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;