10 Kunena za cipulumutso ici anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za cisomo cikudzerani;
11 ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakucitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero, worsarana nao.
12 Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kucokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
13 Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu;
14 monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;
15 komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;
16 popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.