5 amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa cikhulupiriro, kufikira cipulumutso cokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
6 M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,
7 kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;
8 amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi, cimwemwe cosaneneka, ndi ca ulemerero:
9 ndi kulandira citsiriziro ca cikhulupiriro canu, ndico cipulumutso ca moyo wanu.
10 Kunena za cipulumutso ici anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za cisomo cikudzerani;
11 ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakucitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero, worsarana nao.