10 inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira cifundo, koma tsopano mwalandira cifundo.
11 Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zicita nkhondo pa moyo;
12 ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ocita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona nchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
13 Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, cifukwa ca Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;
14 kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ocira zoipa, koma kusimba ocita zabwino.
15 Pakuti cifuniro ca Mulungu citere, kuti ndi kucita zabwino mukatontholetse cipulukiro ca anthu opusa;
16 monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga cobisira coipa, koma ngati akapolo a Mulungu.