16 monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga cobisira coipa, koma ngati akapolo a Mulungu.
17 Citirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Citirani mfumu ulemu.
18 Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.
19 Pakuti ici ndi cisomo ngati munthu, cifukwa ca cikumbu mtima pa Mulungu alola zacisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.
20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pocimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pocita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko cisomo pa Mulungu.
21 Pakuti kudzacita ici mwaitanidwa; 1 pakutinso Kristu anamva zowawa m'malo mwanu, 2 nakusiyirani citsanzo kuti mnkalondole mapazi ace;
22 3 amene sanacita cimo, ndipo m'kamwa mwace sicinapezedwa cinyengo;