2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda cinyengo, kuti mukakule nao kufikira cipulumutso;
3 ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;
4 amene pakudza kwa iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,
5 inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,
6 Cifukwa kwalembedwa m'lembo,Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangondya, wosankhika, wa mtengo wace;Ndipo wokhulupirira iye sadzanyazitsidwa.
7 Kwa inu tsono akukhulupira, ali wa mtengo wace; koma kwa iwo osakhulupira,Mwala umene omangawo anaukana,Womwewo unayesedwa mutu wa pangondya;
8 ndipo,Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa;kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.