1 CIMENE cinaliko kuyambira paciyambi, cimene tidacimva, cimene tidaciona m'maso mwathu, cimene tidacipenyerera, ndipo manja athu adacigwira ca Mau a moyo,
2 (ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo ticita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife);
3 cimene tidaciona, ndipo tidacimva, tikulatikirani inunso, kuti inunso mukayaniane pamodzi ndi ife; ndipo ciyanjano cathu cirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wace Yesu Kristu;
4 ndipo izi tilemba ife, kuti cimwemwe cathu cikwaniridwe.
5 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima.