1 Yohane 3 BL92

Ife ndife ana a Mulungu

1 Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira iye.

2 Okondedwa, tsopano riri ana a Mulungu, ndipo sicinaoneke cimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka iye, tidzakhala ofanana ndi iye, Pakuti tidzamuona iye monga ali.

3 Ndipo yense wakukhala naco ciyembekezo ici pa iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

4 Yense wakucita cimo acitanso kusayeruzika; ndipo cimo ndilo kusayeruzika.

5 Ndipo mudziwa kuti iyeyu anaonekera kudzacotsa macimo; ndipo mwa Iye mulibe cimo.

6 Yense wakukhala mwa iye sacimwa; yense wakucimwa sanamuona iye, ndipo sanamdziwa iye.

7 Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakucita colungama af wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:

8 iye wocita cimo ali wocokera mwa mdierekezi, cifukwa mdierekezi amacimwa kuyambira paciyambi. Kukacita ici Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge nchito za mdierekezi,

9 Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu.

10 M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosacita cilungamo siali wocokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wace.

11 Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace:

12 osati monga Kaini anali wocokera mwa woipayo, namupha mbale wace. Ndipo anamupha iye cifukwa ninji? Popeza nchiro zace zinali zoipa, ndi za mbaie wace zolungama.

13 Musazizwe, abale, Jikadana nanu dziko lapansi.

14 Ife tidziwa kuti tacokera kuturuka muimfa kulowa m'moyo, cifukwa tikondana ndi abale iye amene sakonda akhala muimfa.

15 Yense wakudana ndi mbale wace ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kun wakupha munthu ali yense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.

16 Umo tizindikira cikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wace cifukwa ca ife; ndipo ife tiyener kupereka moyo wathu cifukwa ca abale.

17 Koma iye amene ali naco coma ca dziko lapansi, naona mbale wace ali wosowa ndi kutsekereza cifundo cace pommana iye, nanga cikondi ca Mulungu cikhala mwa iye bwanji?

18 Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kucita ndi m'coonadi.

19 Umo tidzazindikira kuti tiri ocokera m'coonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pace,

20 1 m'mene monse mtima wathu utitsutsa; cifukwa Mulungu ali wamkuru woposa mitima yathu, nazindikira zonse.

21 Okondedwa, 2 mtima wathu ukapanda kuritsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu;

22 ndipo 3 cimene ciri conse tipempha, tilandira kwa iye, cifukwa tisunga malamulo ace, ndipo ticita zomkondweretsa pamaso pace.

23 Ndipo 4 Lamulo lace ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wace Yesu Kristu, ndi 5 kukondana wina ndi mnzace, monga anatilamulira.

24 Ndipo 6 munthu amene asunga malamulo ace akhala mwa iye, ndi iye mwa munthuyo. Ndipo 7 m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kucokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.

Mitu

1 2 3 4 5