1 Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati icokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anaturuka kulowa m'dziko lapansi.
2 M'menemo muzindikira Mzimu Wl Mulungu: mzimu uli wonse umen ubvomereza kuti Yesu Kristu ana dza m'thupi, ucokera mwa. Mulungu
3 ndipo mzimu uli wonse umen subvomereza Yesu sucokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzirm wa wokana Kristu umene mudamvi kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,
4 Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo ocoken m'dziko lapansi;
5 mwa ici alankhula monga ocokera m'dziko lapansi, ndipo dziko tapansi liwamve ra.
6 Ife ndife ocokera mwa Mu lungu; iye amene azindikira Mu lungu atimvera; iye wosacoken mwa Mulungu satimvera ife. Mo mwemo tizindikira mzimu wa coonadi, ndi mzimu wa cisokeretso.
7 Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,
8 iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.
9 Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.
10 Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.
11 Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo
12 Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife;
13 m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace.
14 Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
15 Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.
16 Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
17 M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.
18 Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.
19 Tikonda ife, cifukwa anayamba iye kutikonda.
20 Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.
21 Ndipo lamulo ili tiri nalo locokera kwa iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wace.