1 Yohane 5 BL92

Za kukhulupirira Yesu ndi zotsatira zace

1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu wabadwa kucokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wocokera mwa iye.

2 Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kucita malamulo ace.

3 Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa.

4 Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu.

5 Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu

6 iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi; ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi.

7 Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi,

8 Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.

9 Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; cifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anacita umboni za Mwana wace.

10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace.

11 Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace.

12 Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

13 Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.

Mphamvu ya kupemphera

14 Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera;

15 ndipo ngati tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye.

16 Wina akaona mbale wace alikucimwa cimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo iye adzampatsira moyo wa iwo akucita macimo osati a kuimfa. Pali cimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.

17 Cosalungama ciri conse ciri ucimo; ndipo pali cimo losati la kuimfa.

18 Tidziwa kuti yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacimwa, koma iye wobadwa kucokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

19 Tidziwa kuti tiri ife ocokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

20 Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife cidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tiri mwa Woonayo, mwa Mwana wace Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.

21 Tiana, 1 dzisungireni nokha kupewa mafano.

Mitu

1 2 3 4 5