1 Yohane 2 BL92

1 Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musacimwe. Ndipo akacimwa wina, Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama;

2 ndipo iye ndiye ciombolo ca macimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

Za kusunga malamulo, kukondana, ndi kudzimana zapadziko

3 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira iye, ngati tisunga malamulo ace.

4 Iye wakunena kuti, Ndimdziwa iye, koma wosasunga malamulo ace, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe coonadi;

5 koma iye amene akasunga mau ace, mwa iyeyu zedi cikondi ca Mulungu cathedwa. M'menemo tizindikira kuti tiri mwa iye;

6 iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wace kuyenda monga anayenda Iyeyo.

7 Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa ciyambi; Lamulo Iakaielo ndilo mau amene mudawamva.

8 Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndico cimene ciri coona mwa iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala,

9 iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wace, ali mumdima kufikira tsopane lino.

10 Iye amene akonda mbale wace akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe cokhumudwitsa.

11 Koma iye wakumuda mbale wace ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ace.

12 Ndikulemberani, tiana, popeza macimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lace.

13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambir paciyambi. Ndikulemberani anyamata, popeza mwamlaka woipavo, Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambira paciyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muti amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.

15 Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko apansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, cikondi ca Atate lsiciri mwa iye.

16 Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.

Za okana Kristu

18 Ana inu, ndi nthawi yorsirtza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana. Krisru akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ici tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.

19 Anaturuka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero 1 kuti aonekere kutr sali onse a ife.

20 Ndipo 2 inu muti nako kudzoza kocokera kwa Woyerayo, ndipo 3 mudziwa zonse.

21 Sindinakulemberam cifukwa simudziwa coonadi, koma cifukwa muddziwa, ndi cifukwa kulibe bodza locokera kwa coonadi.

22 4 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Kristu? iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.

23 5 Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wobvomereza Mwana ali ndi Atatenso.

24 Koma inu, cimene munacimva kuyambira paciyambi cikhale mwa Inu, 6 Ngari cikhala mwa inu cimene mudacimva kuyambira paciyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.

25 Ndipo 7 ili ndi lonjezano iye anatiloniezera ife, ndiwo moyo wosatha.

26 Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

27 Ndipo inu, 8 kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza kwace kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.

28 Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa iye; kuti 10 akaonekere iye tikakhale nako kulimbika mtima, osacita manyazi kwa iye pa kudza kwace.

29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti 11 ali yensenso wakucita cilungamo abadwa kucokera mwa iye.

Mitu

1 2 3 4 5