20 Koma m'nyumba yaikuru simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.
21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala cotengera ca kuulemu, copatulidwa, coyenera kucita naco Mbuye, cokonzera nchito yonse yabwino.
22 Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate cilungamo, cikhulupiriro, cikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
23 Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.
24 Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kucita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,
25 1 wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; 2 ngati kapena Mulungu awapatse iwo citembenuziro, kukazindikira coonadi,
26 ndipo 3 akadzipulumutse ku msampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, ku cifuniro cace.