8 Kumbukila Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wocokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;
9 m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wocita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.
10 Mwa ici ndipirira zonse, cifukwa ca osankhika, kuti iwonso akapeze cipulumutsoeo ca mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.
11 Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi iye, tidzakhalanso moyo ndi iye:
12 ngati ttpirira, tidzacitanso ufumu ndi iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:
13 ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha.
14 Uwakumbutse izi, ndi kuwacitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asacite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.