14 Koma munacita bwino kuti munayanjana nane m'cisautso canga.
15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'ciyambi ca Uthenga Wabwino, pamene ndinacoka kuturuka m'Makedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a copereka ndi colandira; koma inu nokha;
16 pakuti m'Tesalonikanso munanditumizira pa cosowa canga kamodzi kapena kawiri.
17 Sikunena kuti nditsata coperekaco, komatu nditsata cipatsocakucurukira ku ciwerengero canu.
18 Koma ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidacokera kwanu, mnunkho wa pfungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu.
20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero ku nthawi za nthawi, Amen.