15 amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse;
16 pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.
17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.
18 Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba.
19 Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire,
20 mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.
21 Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'cifuwa canu m'nchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani