4 kwa Tito, mwana wanga weni weni monga mwa cikhulupiriro ca ife tonse: Cisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Mpulumutsi wathu.
5 Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;
6 ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.
7 Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;
8 komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
9 wogwira mau okhulupirika monga mwa ciphunzitso, kuti akakhoze kucenjeza m'ciphunzitso colamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.
10 Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pace, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe,