2 Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wobvala mphete yagolidi, ndi cobvala cokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi cobvala codetsa:
3 ndipo mukapenyerera iye wobvala cokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;
4 kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?
5 Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi cikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonieza kwa iwo akumkonda iye?
6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu acuma, nakukokerani iwowa ku mabwalo a mirandu?
7 Kodi sacitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?
8 Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino: